Tuesday, September 17, 2024
Government BusinessNews

Nduna ya zachuma ichotsana chimbenene ndi kafuyefuye wolowetsa ndale pankhani yazachuma

Sosten Gwengwe:
Nduna yoona zachuma, olemekezeka Sosten Gwengwe, yati dziko la Malawi silidalandire ndalama yokwana US$6.8 billion (K7 trillion) kuchoka ku Bridgin Foundation.
Gwengwe wati sizoona kunena kuti thumba la boma la Malawi ‘kwalowa’ US$6.8 trillion, ponena kuti kusainila ndikulandira ndalama ndi zinthu ziwiri zosiyana.
“It is truly irresponsible to allege that ‘kwalowa’ US$6.8bn from Bridgin. Signing is different from disbursement. Raising propaganda in an activity as important as budget consultation is indeed nonsensical. Period!!!!,” Watero Gwengwe pa tsamba lake la mchezo la WhatsApp.
Ku nkumano omwe anthu ndi mabungwe osiyanasiyana amapereka maganizo awo kuti pachitike chiyani kuti ndondomeko ya chuma ya chaka cha 2023/2024 iyende bwino, bambo wina osadziwika bwino adafunsa funso kuti nchifukwa chiyani ndalama zomwe boma la Malawi lidalandira kuchokera ku bungwe la Bridgin sizidawoneke bwino-bwino.
Iye adaonjezera kuti ku unduna wa zachuma kukukhala ngati anthu ake sanapite ku sukulu chifukwa cha ziganizo zina zomwe akupanga.
Poyankha fundo yomwe imawoneka kuti ndi wupo (propaganda), aGwengwe adati; “Kulibe anasainira kuti kwabwera ndalama 6.8 billion chani-chani-chani… that’s just nonsense, the real issues are the ones we are talking about. Osati kudzangosewera kuti BRIDGIN foundation, eh chani-chani-chani that’s nonsense, put it aside,”.
Izi zachititsa kuti anthu aganize kuti mgwirizano-wu palibenso ndipo za mgwirizano-wo zinali za bodza. Koma Gwengwe wati mgwirizano ndi Bridgin ukadalipobe koma kufunsidwa kwa funso linafunsidwalo ku Malo woti anthu akukambirana za ndondomeko ya chuma cha dziko kunali kosayenera.
Editor In-Chief
the authorEditor In-Chief