Thursday, March 6, 2025
FeatureNational

‘Peter Mutharika angadzaname, age limit Bill sidutsa,’ Yatero MCP

Aging Mutharika

Zochititsa chidwi kwambiri. Chipani cholamula Boma cha Malawi Congress Party (MCP) chanena monenetsa kuti Bill imene ikufuna kuletsa nkhalamba ngati Peter Mutharika kuima nawo pachisankho cha u President sidutsa ku Parliament ikabwera kunena kuti iwo sakufuna anthu awone ngati kuti MCP ikuopa Peter Mutharika amene ali agogo wotheratu kuti ayime nawo pachisankhochi.

Iwo ati MCP ili ndi a Phungu ambiri mu nyumba yamalamulo ndipo awonetsetsa kuti aphungu asovotere Bill imeneyi kuti idutse pakuti cholinga chawo ndikufuna kukwapulaso Peter Mutharika kachiwiri mu Chisankho chimene chili kubwela mu September Chaka Chino.

“Munthu amene mutu wake ukuyenda bwino sangovotere nkhalamba Peter Mutharika kuti izikagona ku state house pamene achina Chisale, Getu and Mukhitho akupitilira kusakaza chuma cha dziko lino monga m’mene ankachitira muja.”

“Ndiye tikumufuna Peter Mutharikayo kuti ayime kuti adzaone polekera ataluza,” atero akulu-akulu a MCP.

Editor In-Chief
the authorEditor In-Chief