Lero anabwata mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazaraus Chakwera ndithudi kuyaka moto kuti buu pamene anauza khamu limene linasonkhana kumeneko kut palibe amene angamuchotse m’boma pogwiritsa ntchito mabodza.
Dr Chakwera wayankhula izi lero pa mwambo otsegulira makina apamwamba a kampani ya Coca Cola Beverages Malawi Limited ku Kanengo mu mzinda wa Lilongwe, omwe azipanga zokumwa za m’maboto a pulasitiki.
Mtsogoleri wa dziko linoyu wati zoti m’Malawi muno mulibe ndalama ndi zabodza ndipo zikufalitsidwa kwambiri ndi anthu otsutsa boma.
“Ripoti la posachedwapa la banki yaikulu m’dziko muno ya Reserve, la momwe aMalawi akumatumizirana ndalama zolipilira zinthu zosiyanasiyana, lawonetsa kuti chaka chatha aMalawi anatumizirana ndalama zosachepera K19.5 trillion kudzera ku Airtel money komaso TNM Mpamba, ndalama zomwe zipotsa budget ya boma ya chaka chino yomwe ndi yandalama zokwana K8 trillion, chitsimikizo choti m’dziko muno muli ndalama zambili.
Mtsogoleriyu watinso anthu ambiri m’dziko muno akapeza ndalama amazigwiritsa ntchito molakwika kenako kuyamba kukopeka ndi anthu andale otsutsa boma omwe akulodza dzala boma la a Chakwera kuti ndi lomwe likusaukitsa anthu.
Apa Dr Chakwera wayamikiranso kampani ya Coca Cola kuno ku Malawi kaamba kokhala mbali imodzi yopititsa patsogolo chuma cha dziko lino.