Wednesday, February 26, 2025
GeneralNewsPolitics

“Inu tinathana nanu kale”, ma venda amasula ma MP aDPP lero ku Lilongwe

 

Ma MP asanu ndim’modzi otsutsa boma achipani cha DPP anadziyenereza kuti iwo ndioyenera kulankhula ma vendor amene anasonkhana ku Parliament kukapereka madando awo. Koma ma vendor anawakana movetsa chisoni amvekere “inu ndiye mukudzatani, tikufuna amene tinawaika m’boma atilankhule, inu tinakuchotsani kale m’boma chifukwa cha kusamva kwanu ndipo mukhalabe kotsutsa mpakana mudzalape machimo anu kwa a Malawi.”

Ma MP wo, omwe maina awo ndi aBen Phiri; aShadrick Namalomba; aSameer Suleman, aVictor Musowa; aCharles Mchacha, komanso aNoel Lipipa anachita nyotcholi ngati anapiye onyowa ndi matsukwa ndi kubwelela mwa manyazi mu parliamentary chamber.

Kenako nduna ya boma Sosten Gwengwe yinatulukira ndikuwalankhula ma vendor wo powatsimikizira kuti boma lawo lili nawo ndipo awathandiza kuti chipongwe chimene akulandila kwa a mwenye ndi ma china kumangokweza mitengo ya ma belo ya zovala mwachisawawa lithe.

Pakadali pano, ndunayo yalanda ziphaso zochitira malonda kwa anthu awupanduwa kuti vendor ndi anthu a M’malawi muno atetezedwe.

Editor In-Chief
the authorEditor In-Chief