Saturday, December 21, 2024
Law and orderNews

Boma lamanga obela anthu ndalama popeleka ziphaso zawo zaunzika

A Nelson Banda a zaka 42 ali m’manja mwa apolisi ku Nkhotakota atapezeka akugawa ziphanso za unzika zokwana 200 kwa anthu ena m’dera la Mapala kwa mfumu Nkhanga m’bomali.

A Banda akuti amauza eni ziphansozo kuti alipire ndalama yokwana K500 kapena K300 ngati akufuna kutenga chiphaso chawo.

M’neneri wa polisiyo, a Paul Malimwe, ati sangatsimikize ngati bamboyo ndi m’modzi mwa anthu omwe akuwonelera nawo kalembera (monitor) wa chisankho m’bomali.

A Malimwe ati lipoti lomwe bamboyo wapereka akuti ziphasozo anapatsidwa ndi m’modzi mwa aphunzitsi pa sukulu ya pulayimale ya Kasipa kwa mfumu Mwadzama kuti akapereke pa sukulu ya Mapala chifukwa anthu ake anali adelaro.

“M’malo mopereka ziphaso pa sukuluyo, a Banda anayamba kugawa pawokha ndiye ife apolisi komanso a nthambi yomwe imachita kalembera wa unzika ya NRB tikuchitabe kafukufuku pa nkhaniyi,” atero a Malimwe.

A Nelson Banda akuwasunga pa polisi yaying’ono ya Mkaika m’bomali.

Editor In-Chief
the authorEditor In-Chief