Wednesday, December 18, 2024
News

Page Hacking Scandal: DPP Yakonza Zotumiza Nthumwi ku Facebook Headquaters Kukachondelera kuti Abwezeletse Page Yomwe Yapangidwa Hack

 

Chipani cha DPP chazunguzika mutu kutsatila chipongwe chomwe chalandira sabata ino pamene page yachipanichi pa Facebook yapangidwa hack.

Kunali mpungwe-pungwe kunkumano wa DPP omwe umachitikira pa Whatsapp komwe amakambirana zavutoli.

Malinga ndimalipoti omwe Shire Times yalandira kuchokera kwa ena omwe anali nawo pankumanowu, akuti page yomwe yachitidwa chipongweyi imayendetsedwa ndi anthu atatu omwe mayina awo ndi Shadrick Namalomba; Emmanuel Matewere komanso njonda ina yomwe imakhala ku South Africa ndipo ikugwiritsa ntchito phone number iyi yomwe inapangwidwa register ku France: +33 7 53 83 20 70 ndipo pagulupo amadzitcha kuti KTC.

KTC yu akuti amadzitchula kuti ndi katswiri waza social media komanso internet in general (whatever that means).

Ndipo akulu akulu achipanichi apanga chiganizo kuti mtsikana wina yemwe amatchuka kuti Phoebe Kachala, ndipo amakhala ku America, anyamuke apite ku headquarters ya Facebook kukachondelela kuti page yachipanichi ayibwezeletse mchimake. Pakali pano akulu akuluwa akuchita msonkha-sonkha wandalama kuti amutumizire Kachala kuti agwilire ntchito yomwe amutumayo.

Koma izi zinamuseketsa KTC yemwe amadzitchula kuti ndikatswiriyo ndipo anawaseka omwe anabweletsa maganizo amenewa ponena mawu awa: “Akuti Phoebe apite ku Facebook headquarters akachondelere kuti the page must be returned…be serious plz”.

Kafukufuku wina yemwe Shire Times yachita akusonyeza kuti m’mbuyomo page yachipanichi imayendetsedwa kwambiri ndi nkulu wina (otipatsa nkhaniyi sanamutchule kupatula kutnena kuti) ankagwira ntchito ku Bank mu Mzinda wa Lilongwe koma adathotholedwa ndi Emmanuel Matewele.

Pakali pano, nkhani yamutsalira Matewere yemwe wakhadzulidwa kodetsa nkhawa ndi njonda ina yotchedwa Edmond yomwe imakhala ku South Africa. Edmond wamuwuza Matewere kuti ndi mbuli ndipo alibe kuthekela koyendetsela page yachipani. Koma Matewere sanamwetulire polandila chipongwechi pakuti wachenjeza makosana omwe akumuloza zalawa kuti amusamale akhoza kuika zinthu zambiri pam’mbalanganda.

 

 

Editor In-Chief
the authorEditor In-Chief