Ndikhulupilira kuti aMalawi tonse tikukumbukira kuti kuyambira mu chaka cha 2014 pamene a Peter Mutharika adalowa m’boma ngati mtsogoleri wadziko lino, anthu a khungu la chi alubino adasanduka nyama zakuthengo zomwe zimaphedwa ngati agwape. Zomvetsa chisoni.
Moyo wa anthu achi-alubino udafika pachiwopsyezo komanso omvetsa chisoni kwambiri powasandutsa mpamba wadziwenga dzopanda chisoni. Amadulidwa ziwalo mkumakagulitsa. Ndi nkhani yomvetsa chisoni kwambiri.
Pa 31 December mu chaka cha 2018, zigawenga zokwana 8 zidapita kunyumba ya aYasini Phiri ku NkhataBay usiku ndipo zidawakhapa-khapa kuwapha ndikuwaduladula ziwalo. Nkhanza izi zimachitika pomwe mwana wawo wazaka 9 amawonelera koma mwamwayi mwanayu, yemwe pano akukhala ndi umasiye omwe ndiosayiwalika, sadaphedwe.
Pa 13 February mu2018 momwemo, Goodson Makanjira wa zaka 14 ku Dedza adaphedwa ndizigawenga zomwe zimasaka ma alubino ngati nyama zakuthengozi. Thupi la Goodson lidakapezeka mum’tsinje wa Dyamphwi koma litadulidwa ziwalo zina ndi zina.
Pa 22 January mu2018 momwemo, kamwana kakhanda kotchedwa Eunice Nkhonjera kadabedwa usiku pomwe amagona ndi amayi ake. Pamene mayi ake amadzuka adazindikira kuti mwana wawo palibepo wabedwa. Mpakana pano komwe kudalowela khanda limeneli sikukudziwika koma chomwe chili chachidziwikire ndichakuti khandali lomwe linali lachi alubino lidaphedwa ndi anthu ankhanzawa.
Ma report ankhanza zimenezi amakhala akusindikidwa kumasamba ankhani osiyanasiyana kuphatikizirapo pano pa internet koma boma silimawoneka kuti likuchitapo kanthu pofuna kuthana ndimchitidwewu. Boma lidawayang’anira kumbali abale athu achi-alubino. Akamati oyipa Satana ndyerekezi amabwelera kupha, kuba ndikuwononga, izi tidaziwona mu ulamulira wa oyipawo.
Wina mwa zigawengazi adagwidwa ndi apolisi ena ndipo adamutengera ku court. Ku court ko adatchula akuluakulu am’bona kuphatikizilapo a Hetherwick Ntaba komanso aPeter Mutharika omwe anali mtsogoleri wadziko.
Mkulu winanso yemwe adagwidwa pankhani zomwezi ndikuzengedwa milandu, Buleya Lule, adakonzekera kuti akawulura yemwe amawatuma kuti azichita zinthu zimenezi. Koma usiku wina, pomwe anali mmanja mwa apolisi, aBuleya Lule adachitidwa chipongwe mpakana adafa. Kukhala ngati kufafaniza umboni.
Bambo Nicholas Dausi omwe anali nduna nthawi imeneyo adayankhapo kuti vuto abale anthu achialubinowa lininafike poyipitsitsa kuti mpakana boma limayenela kuchitapo kanthu. Izi adayankha pomwe anthu ena amachita ma demonstrations okakamiza boma kuti lilowelerepo pa chitetezo cha anthu achialubinowa.
Koma akuluakulu akale adanena kale kuti mdima ukachulukitsa ndiye kuti kwatsala pang’ono kucha. Mu chaka cha 2020, utsogoleri wa Dr. Lazarus Chakwera udafika mdziko muno ndipo zigawenga zomwe zimatetezedwa ndi atsogoleri omwe ankalamula dziko kumbuyoko zidasiyilatu ziwembu zawo pozindikira kuti amene amawateteza achotsedwa muboma.
Mwachanguchangu, boma laChakwera lidamanga nyumba zotetezeka zokwanila 28 zomwe adazipeleka kumabanja omwe ali ndi anthu achialubino. Izi boma lidachita pozindikira kuti nyumba zomwe zigawenga zimalowa nkukapanga chipongwe anthu achialubinowa zinali nyumba zosoweka chitetezo. Kuphatikizila apo, boma lidalamula apolisi kuti agwire ntchito kosaphethira komanso kosapumira pothana ndizigawenga zomwe zimapha alubino. Kuyambira pomwepo, zigawengazi zidasiya mchitidwe wonunkhawo ndipo tikunena pano anthu achialubino akuyenda komanso kugona mwaufulu mopandanchewuchewu.