Wednesday, March 26, 2025
FeatureNational

Utsogoleri koma wa Chakwera; anthu osokoneza ziwonetsero ku Lilongwe awona polekera

Utsogoleri koma uwu. Chakwera adadzuka ndi mkwiyo ndikulamula kuti amene akuchita chipolowe kuletsa azawo kuti asapange ziwonetsero afufuzidwe ndi a Police komanso amangidwe. Anthu amati anthuwo ndi a MCP. Izi zilibe umboni. Zimene zili ndi umboni ndi zakuti anthu angapo amangidwa pokhudzana ndi nkhani imeneyi ndipo lamulo likugwira ntchito.

Utsogoleri koma umenewu chifukwa tinaonako utsogoleri wachabe. Ma Alubino kuphedwa president osachitapo kanthu. Anthu kumenyedwa ku mmwera achina Billy Mayaya a Police osachitapo kanthu. Chakwera ndi wina wina. Zopusa sapanga nawo.

Ngati tikufuna President, look no further. President ndi yemweyu.

Editor In-Chief
the authorEditor In-Chief