Anthu odziwa ndale ndi utsogoleri akamati Dr. Lazarus Chakwera awinanso, timenane izi: Taganiza, ma vendor kapena kuti ochita malonda osiyanasiyana mu m’misika ya mu mzinda wa Mzuzu zimene anena. Ndiye mudzifunse kuti izi zikutanthauza chiyani. Ma vendor a ku Mzuzu awuza President Dr. Lazarus Chakwera kuti iwo sakudana ndi utsogoleri wa Pulezidentiyu ayi ndipo ati iwo ndiwodzipereka kwathunthu kuthandiza boma lake kutukula Malawi.
Ochita malondawa alankhula izi lero lachiwiri pa 4 March 2025, pomwe anakumana ndi Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus McCarthy Chakwera kunyumba yaboma ya Mzuzu State Lodge.
Polankhula kudzera mwa mtsogoleri wawo, Gerald Maulana, ochita malondawa ati atamva kuti Mtsogoleri wa dziko wawayitana kuti akakambirane zokhudza umoyo wawo, iwo anachiwona cha nzeru kuti ayimitse chikonzero chawo chofuna kuchita ziwonetsero pofuna kupereka nkhawa zawo kwa Mtsogoleriyu, ndipo kuti mmalo mwake akumane naye ndikutula nkhawa zawozi.
“Sitikudana ndi utsogoleri wanu, ndipo mukationa tikulira, muzidziwa kuti tili ndi madando ofuna inu mulowererepo monga tate wathu. Ndiye titamva kuti inu mwavomera kukumana nafe lero, panalibenso chifukwa choti ife tikayendere pa nsewu kukatula nkhawa zathu kukhonsolo, mmalo modzapereka kwa inu. Inu ndinu Mtsogoleri owopa Mulungu mchifukwa chake adakuyikani pampando panthawi yomwe dziko lathu likudutsa mmavuto ochuluka” anatsindika motero mtsogoleri wa ochita malondayu.
A Maula anathokonzanso Pulezidenti Dr Chakwera kamba kolowererapo nsanga madandaulo okhudza ochita malonda a Kaunjika mdziko muno, ponena kuti ichi mchitsimikizo kuti Mtsogoleriyu amayika zofuna za ochita malondawa pamtima pake.
Anthu akamati DPP anthu adathana nayo, amanena zinthu ngati zimenezi. Anthu akamati Boma ndi lomweli amanena zinthu ngati zimenezi kuti atha kulidzudzula boma lawo koma izi sizikutanthauza kuti sadzalivotera koma pakuti opposition idachepa mphamvu, amafuna azitsutsa okha boma pamene zikulakwika popeza boma ndi lomweli. Palibeso lina.