Sunday, January 19, 2025
EXCLUSSIVEGeneralInnovation and TechnologyNationalNewsPoliticsState Affairs Records

President Chakwera watumiza Usi kukagawa chimanga ku constituency ya Mwanamveka

 

Pomwe boma, pansi pa mtsogoleri Dr. Lazarus Chakwera, likupitilirabe ndikugawa chimanga kwa anthu omwe akhudzidwa ndinjala madela osiyanasiyana, lero anatumiza wachiwiri wake aMichael Usi omwenso ali nduna ya Boma yowona ndondomeko yopeleka chitukuko komanso zinthu zosiyanasiyana (Minister of State for Public Service Delivery) pamodzi ndi nthambi yaboma ya Department of Disaster Management Affairs (DODMA) kukagawa chimanga kwa anthu aku constituency yomwe imayimilidwa ndi phungu otsutsa boma wa DPP a Joseph Mwanamveka.

Popeleka chithandizochi, Dr. Michael Usi analankhulako pazam’chitidwe wauchifwamba omwe anthu ena otsutsa boma achipani cha DPP akhala akuyankhula komanso kuchita potsekela malire anthu achipani cholamula cha Malawi Congress Party (MCP) kumadela kwawo. Dr. Usi anati m’chitidwe wodulirana malire chifukwa cha ndale ndi moyo wa chi kalekale.

Wachiwili kwa mtsogoleriyu wati kupatula mchitidwewu kubweletsa kusamvana mdziko, izi ndi zimene zakhala zikubwezeretsa m’mbuyo chitukuko cha dziko lino.

“Kodi ngati a zibambo pofusira banja sitimafunsa kuti mkaziyo ndi wa chipani chanji, bwanji timalimbana ndi kudulirana malire kuti chigawo ichi ndi cha chipani chakuti ndipo a chipani ichi sangapiteko kapena kupangako chitukuko”, anayankhula motele Dr. Usi poonetsa kudabwa.

Iwo ayankhula izi lero pomwe amapereka chimanga kwa mawanja 59 m’mudzi wa Musa mfumu yaikulu Nkalo m’boma la Chiradzulu omwe poyamba amakhala m’mudzi wa Mtauchira omwe unakhudzika ndi vuto la ku sefukira kwa madzi a namondwe Freddy mchaka cha 2022.

Phungu wa derali a Joseph Mwanamvekha a chipani chotsutsa cha DPP, wayamikira wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu kamba ka thandizoli ponena kuti ambiri mwa mawanjawa adakakumanabe ndi vuto la njala ngoziyi chichitikileni.

 

 

Editor In-Chief
the authorEditor In-Chief