Anthu akuti ndizosangalatsa kuti President Chakwera akuyika anthu ofunikira m’malo mwawo tsopano. Anthu ochuluka anena izi pamene nduna yatsopano yowona za Malonda Wolemekezeka a Vitumbiko Mumba ayamba kutipula pa ground tsopano. A Mumba anatsinidwa khutu kuti store ya Chipiku pa Game Complex Ku Lilongwe ikumabisa sugar nkumauza anthu kuti sugar watha. Kumawauza anthu kuti agule sugar muwiri-muwiri chifukwa kulibe sugar chosecho sugar atamubisa. Ndipo ndi ma shop ambiri akupanga izi, ena atava ukali wa Mumba angophwethula ma bale kumuika mma shop mwawo kuti anthu agule.
Atava izi, a Mumba anapita ku Shop komweko ndikukalowa komwe amabisiko sugar yo kumene anapeza chi phiri cha ma bale a sugar ali neng’a-neng’a. Amumba akuti chikatele ndi chani ichi? Kakasi kusowa zolunkhula amwenye.
Awa ndi amwenye aja Chakwera amanena kuti akugwira ntchito ndi chipani chotsutsa cha DPP kuti chivetse kupweteka a Malawi pobisa sugar, kukweza kaunjika, kukweza ma groceries mosakhala bwino kena kano kuti anthu m’ma social media azingotukwana Chakwera kuti walephera. DPP chipani chachabe, chisadzabweleso! Ndiye alemba m’madzi chifukwa a Mumba ati savomera zachibwana ngati zimenezi kuti zipitilire.