Phungu wa Chikwawa North Owen Chomanika wati iye wayenda nawo bwino a Lazarus Chakwera, ndipo lero wawona kuti ndi chanzeru kuti ayende ndi chipani cha Malawi Congress Party pomwe tikupita ku zisankho.
“A Chakwera ndayenda nawo bwino zedi iwowo anandipatsa unduna, atapangira zitukuko zambiri kuno, ndiye mufuna tisayende nawo? Sikulakwitsa kumeneko? Ndiye ineyo ndipemphe anthu anga kuno kuti m’tsogoleri ndi yemweyu ndipo timusapote,” atero a Chomanika.
A Chomanika panthawi yomwe amawasankha ngati wachiwiri wa nduna anali Phungu wa chipani cha DPP. Iwowa anapatsidwa unduna ndi Boma la Malawi Congress Party, ndipo lero alowa chipanichi.
A Chakwera sakucheza kuitenga DPP half ground ku mmwera ndi cholinga chakuti adzapeze ma vote amene adzawapangitse kuti game idzathere round one akadzakwapula 50% plus one. Kwinaku, DPP ikungolimbana ndikuti iyankha bwanji milandu ya azitsogoleri ake opeza ma certificate a MSCE mwa chinyengo pamene mtsogoleri wawo akugona ndi kuothera dzuwa kunyanja uko chifukwa cha ukalamba.